22/01/2024
MATENDA A NKHUKU.
Tichite mobweleza
1- NEW CASTLE
- Amayambitsidwa ndi virus
- matendawa alibe mankhwala
- Amatetezedwa popatsa katemera nkhuku zanu
ZIZINDIKIRO
- Kubiba bibi la madzi kwambiri komaso bibi la green
- kutulutsa thovu,madzi olenda mkamwa ndi mphuno kutchula zochepa
Chitopa chimapha nkhuku zochuluka pakodzi
Chimafala kuchokera Ku nkhuku kupita Ku nkhuku popumirana,muzomwera madzi ndi zodyero,atambara amafalitsaso
GUMBORO
- Amayambitsidwa ndi Virus
-Alibe mankhwala
-Amatetezedwa ndi katemera
ZIZINDIKIRO
-Nkhuku zimabiba bibi loyera
-Zimakana kudya
-Nthenga zimanyankhalara
- Nkhuku zimafa mkati kati mwa masiku atatu.
-Anapiye a ma week atatu mpakana six amakhaka pa chiopsezo.
*mwina mwa yankhidwa madandaulo anu okhudza kufa ifa kwa anapiye ,paja ambiri mumadadaula kuti anapiye anga akungofa.
FOWL POX (ZIRONDA)
-Zimayambitsidwa ndi virus
-Zilonda zitha kupola ngati mafulumiza mankhwala
-Zimatetezedwa ndi katemera
MWATENDA OCHIZIKA
INFECTIOUS CORYZA (chifuwa)
ZIZINDIKIRO
-Kutupa mutu ndi nkhope
-mmaso mumatuluka zoyera ngati nsima
-zimachira ndi OTC
-Chotsani nkhuku zose zodwala
Amayambitsidwa ndi bacteria
INFECTIOUS BRONCHITIS
(Chinfine)
-Chimayambitsidwa ndi bacteria
ZIZINDIKIRO
-Kuyetsemura,kukhosomira
-kutuluka mamina mphuni,mkamwa ndi misonzi mmaso
-zimachira ndi antibiotics
COCCIDIOSIS (kamwanzi)
-Amayambitsidwa ndi bacteria
ZIZINDIKIRO
-BIbi lophatikiza ndiagazi
- nkhuku siidya
-Imapepuka
-Zimachira ndi Triple Sulphur
Kapena Amprolium
NJOKA ZA MMIMBA
-ZImayambitsidwa ndi nyongolotsi
-mankhwala ake ndi Peperazine
Kwalero tiime p***a
Next katemera ndi nthawi yake.