Malawi Muslim Singles

Malawi Muslim Singles WORKING ON

09/05/2026

Once upon a time, there used to be a group of educated well to do women with good jobs who used to meet every Friday Ati going for enjoyments just to show their husbands that they’re capable of doing exactly what a man can do. Khaya zinathera kuti. A few I know are divorced.
As a woman don’t compare yourself with a man. Men cheats everyday, when caught what happens? “Heee he’s a man, it’s their nature, blah blah blah”
When it’s a woman’s turn; “ndahule aja inu!”
Let’s just know our responsibility and limits as women.
A man can get divorced today with 7 kids and still get married the next month. A woman when divorced with 3kids the same men who used to admire her ali pa banja becomes so hesitant even texting her. Finding a man to take care of your emotions and accept your kids becomes a challenge.
Let’s be careful with our circle of friends and what we teach each other. Pena kumayendako ngati chiweto opanda magulu magulu, sikupepera koma kudziwa chomwe uli.
Circle ya ine ndi imbwa yanga Lmt Adonai Reigns daily imathera ma penalty but we are glued together coz timadzudzulana mosabisilana mau.
Have a blessed Saturday.

09/05/2026

As Salaam Alykum Warahmatullahi Wabarakaatuh

Ma Single Anzanga Kwacha Bwanji Komwe Muliko

09/05/2026

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Yamikan Mpeusa, Amina Ayden, Hainabu Piyo, Osagei Jefry Sanud, M***a Mchebe, Shaibu Nelson, Hajira Chama, Hazey Fred, Hawa Juma, M***aa Sadiqe, Taonga Mbewe, Franque Antonio

05/05/2026

TINGATANI KUTI TIMANGE BANJA LATHU

Kumanga banja losangalala si zamatsenga, ndi ntchito ya tsiku ndi tsiku kuchokera kwa onse awiri. Kaya mu Islam kapena mwambiri, mfundo zazikulu ndizofanana.

*Momwe mungamangire banja losangalala:*

- *Kulankhulana momasuka*: Lankhulani za zonse. Zosangalatsa, zokhumudwitsa, mantha, maloto. Musayembekezere kuti mnzanu awerenge maganizo anu.
- *Ulemu*: Muzilemekezana ngakhale simukugwirizana. Palibe kutukwana, kunyoza, kapena kunyozetsa pamaso pa anthu ena.
- *Chikondi & Chifundo*: Mtumiki ﷺ anali wachikondi ndi akazi ake. Muzichitana zinthu zazing'ono zosonyeza chikondi. _“Abwino mwa inu ndi omwe ali abwino kwa akazi awo.”_ Hadith
- *Kukhululukirana*: Palibe munthu wangwiro. Muphunzira kukhululuka msanga osasunga chakukhosi.
- *Kuthandizana*: Banja ndi mgwirizano. Thandizanani pa ntchito za panyumba, ndalama, kulera ana. Musati “zimenezo ndi ntchito ya mkazi/mwamuna.”
- *Kupembedza limodzi*: Mu Islam, kupemphera limodzi, kuwerenga Qur’an, ndi kupanga dua limodzi kumalimbitsa ubale. Mumayandikira kwa Allah pamodzi.
- *Nthawi yanu*: Muzipangana nthawi yokhala awiri okha. Osalola ana, ntchito, kapena foni zitenge nthawi yanu yonse.
- *Kuyamikira*: Muzithokoza mnzanu ngakhale pazinthu zazing'ono. “Zikomo pophika” zimamanga mtima.
- *Kuthetsa mikangano mwanzeru*: Musamakangane mukakwiya. Pumulani kaye, kenako kambiranani. Vuto liwukireni, osati munthu.

Muchisilamu mwachindunji:
Kumbukirani kuti mkazi/mwamuna wanu ndi _amanah_, chinthu chosungidwa chimene Allah adakupatsani. Mudzayankha za momwe mudawasamalira.

04/05/2026

Osaiwala Kuti Ndizotheka Mkazi Kumuuza Mamuna Amene Akumuona Kuti Ndiolongosoka Ndi Deen Yake Kuti Amukwatire Athandizane Kutumikila Allah
Koma Chitani Izi Pogwilisa Ntchito Wachibale Wanu Monga Bambo Anu Kapena Brother Anu Pofuna Kupewa Ma Fitna

04/05/2026

Swalah Ya Fajir Sikuti Ndiswala Chabe Koma Fuel Watsiku Lanu Lonse Yambani Tsiku Lanu Ndi Swalah Ya Fajir,Onani Kusintha.

03/05/2026

Tiyeni Tisiye Kumazinamiza Tokha Nkumaganiza Kuti Tipeza Mkazi Amene Sazafuna Ndalama,
Koditu Chasintha Ndi Liwu La Ndalama Lokhalo Koma Ndikale Lonse Timadziwa Kuti Mamuna Akakhala Waulesi Samalipeza Banja
Mamuna Akakhala Kuti Alibe Munda Banja Samalipeza. Pomwe Masiku Ano Zonse Zija Zapangidwa Replace Ndi Ndalama
Chisilamu Chikumpasa Mamuna Chilolezo Chokhala Ndi Mkazi Pokhapokha Ali Ndi Kuthekera Komusamalira
Mtumiki Salla llahu Alyhi Wasallam Adati;
من استطاع منكم البائة فاليتزوج
Amene Angakwanise Mwainu Kupeza Mphamvu Zomusamalira (Mkazi Kuyambila Kuchipinda, Kumuveka, Kumudyesa Ndikumupezela Malo Ogona) Akwatire.

Ndiye Zonsezo Sizingatheke Popanda Chuma/Ndalama.Ngati Ulibe Zimenezo Mumuope Allah Ndiye Muzisala Pofuna Kuchepesa Zilako Lako Zanu Zathupi.
Allah Atipase Kumvesesa Pa Deen

03/05/2026

Anthu Ambiri Sakuwapeza Ma Banja Chifukwa Chakuziyenereza Kwambiri, Kumaganiza Kuti Moyo Uzawapasa Zonse Zomwe Amazifuna, Koma Moyo Suli Choncho
Asiyat(Mkazi Wafarawo) Anali Mkazi Owopa Kwambiri Mulungu Kuposa Azimayi Onse Anthawi Ya Musa
Koma Anali Pabanja Ndi Mamuna Oyipitsisa Kwambiri Padziko Lonse
Kukhala Ndi Banja Labwino Kapena Ayi Simuyezo Oyezela Kupambana Kwanu Pamaso Pa Allah
Kwakwanila Kwa Mzimayi Kusankha Mamuna Wa Eiman Kukhala Mapeto Azisankho Zake
Allah Atipase Kumvesesa Deen

02/05/2026
02/05/2026

Pamene Tili Munyengo Ya Mayesero Ambiri Chinthu China Chomwe Chikukolezera Ma Fitna Amenewa Ndiko Kuwasala Ma Divorce Komanso Ma Single Mothers
Mtumiki Wa Allah Adati;
Akwatileni Azikazi Omwe Asiyidwa Ma Banja Chifukwa Iwo Amayambisa Mayesero Mumzinda

Mayesero Amabwela Bwanji Iwo Ndi Azimayi Woti Adauzolowela Umoyo Wam'banja (Kudya Daily)
kotero Kukhalisa Ali Pawokha Ndi Fitna Yaikulu Imene Azimuna Wosamuopa Allah Amangowagwilisa Ntchito Nkuwataya Pongotengelapo Mwayi Wa Desperation Yawo
Allah Atiwongole Ndikutipasa Kumvesesa Deen

18/06/2024

Kukhala Admin Wa Malawi Muslim Singles Koma Nkukhalanso Single Uh🙄

Address

Lilongwe

Telephone

+265992677790

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Malawi Muslim Singles posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share